Ezra 2
Mʼndandanda wa Ayuda amene Anabwerera
1Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerako ku ukapolo, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anawagwira ukapolo ndi kupita nawo ku Babuloni (iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wake. 2Iwo anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Seruya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana).Chiwerengero cha anthu aamuna a Israeli chinali chotere:3 ▼
4– 5– 6– 7– 8– 9– 10– 11– 12– 13– 14– 15– 16– 17– 18– 19– 20– ▼Kuti mukonze bwino tebulo lomwe lili m’vesili, pakhala kofunika kusuntha za vesi (ma) 4-Ezr 2:20 m’menemo.
| Zidzukulu za Parosi | 2,172 |
| (4) zidzukulu za Sefatiya | 372 |
| (5) zidzukulu za Ara | 775 |
| (6) zidzukulu za Pahati-Mowabu (zochokera kwa Yesuwa ndi Yowabu) | 2,812 |
| (7) zidzukulu za Elamu | 1,254 |
| (8) zidzukulu za Zatu | 945 |
| (9) zidzukulu za Zakai | 760 |
| (10) zidzukulu za Bani | 642 |
| (11) zidzukulu za Bebai | 623 |
| (12) zidzukulu za Azigadi | 1,222 |
| (13) zidzukulu za Adonikamu | 666 |
| (14) zidzukulu za Bigivai | 2,056 |
| (15) zidzukulu za Adini | 454 |
| (16) zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) | 98 |
| (17) zidzukulu za Bezayi | 323 |
| (18) zidzukulu za Yora | 112 |
| (19) zidzukulu za Hasumu | 223 |
| (20) zidzukulu za Gibari | 95. |
21 ▼
22– 23– 24– 25– 26– 27– 28– 29– 30– 31– 32– 33– 34– 35– ▼Kuti mukonze bwino tebulo lomwe lili m’vesili, pakhala kofunika kusuntha za vesi (ma) 22-Ezr 2:35 m’menemo.
| Anthu a ku Betelehemu | 123 |
| (22) Anthu aamuna a ku Netofa | 56 |
| (23) Anthu aamuna a ku Anatoti | 128 |
| (24) Anthu aamuna a ku Azimaveti | 42 |
| (25) Anthu aamuna a ku Kiriati Yearimu, Kefira ndi Beeroti | 743 |
| (26) Anthu aamuna a ku Rama ndi Geba | 621 |
| (27) Anthu aamuna a ku Mikimasi | 122 |
| (28) Anthu aamuna a ku Beteli ndi Ai | 223 |
| (29) Anthu aamuna a ku Nebo | 52 |
| (30) Anthu aamuna a ku Magaibisi | 156 |
| (31) Anthu aamuna a ku Elamu wina | 1,254 |
| (32) Anthu aamuna a ku Harimu | 320 |
| (33) Anthu aamuna a ku Lodi, Hadidi ndi Ono | 725 |
| (34) Anthu aamuna a ku Yeriko | 345 |
| (35) Anthu aamuna a ku Sena | 3,630. |
36 ▼
37– 38– 39– ▼Kuti mukonze bwino tebulo lomwe lili m’vesili, pakhala kofunika kusuntha za vesi (ma) 37-Ezr 2:39 m’menemo.
Ansembe anali awa: | Zidzukulu za Yedaya (kudzera mu banja la Yesuwa) | 973 |
| (37) Zidzukulu za Imeri | 1,052 |
| (38) Zidzukulu za Pasuri | 1,247 |
| (39) Zidzukulu za Harimu | 1,017. |
42Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:
| Zidzukulu za Salumu, zidzukulu za Ateri, zidzukulu za Talimoni, zidzukulu za Akubu, zidzukulu za Hatita ndi zidzukulu za Sobai | 139. |
43 ▼
44– 45– 46– 47– 48– 49– 50– 51– 52– 53– 54– ▼Kuti mukonze bwino tebulo lomwe lili m’vesili, pakhala kofunika kusuntha za vesi (ma) 44-Ezr 2:54 m’menemo.
Otumikira ku Nyumba ya Mulungu anali awa: | Zidzukulu za |
| Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti, |
| (44) zidzukulu za Kerosi, zidzukulu za Siyaha, Padoni, |
| (45) zidzukulu za Lebana, zidzukulu za Hagaba, zidzukulu za Akubu, |
| (46) zidzukulu za Hagabu, zidzukulu za Salimayi, zidzukulu za Hanani, |
| (47) zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, zidzukulu za Reaya, |
| (48) zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nekoda, zidzukulu za Gazamu, |
| (49) zidzukulu za Uza, zidzukulu za Peseya, zidzukulu za Besai, |
| (50) zidzukulu za Asina, zidzukulu za Meunimu, Nefusimu, |
| (51) zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri, |
| (52) zidzukulu za Baziruti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa, |
| (53) zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema, |
| (54) zidzukulu za Neziya ndi zidzukulu za Hatifa. |
55 ▼
56– 57– 58– 59Anthu ali mʼmunsiwa anabwera kuchokera ku mizinda ya Teli-Mela, Teli-Harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ngakhale samatha kutsimikiza kuti mafuko awo analidi Aisraeli enieni kapena ayi:▼Kuti mukonze bwino tebulo lomwe lili m’vesili, pakhala kofunika kusuntha za vesi (ma) 56-Ezr 2:58 m’menemo.
Zidzukulu za antchito a Solomoni zinali izi: | Zidzukulu za | |
| Sotai, zidzukulu za Hasofereti, zidzukulu za Peruda, | |
| (56) zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli, | |
| (57) zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu, | |
| zidzukulu za Pokereti, Hazebayimu ndi Ami. | |
| (58) Chiwerengero cha onse otumikira ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za Solomoni chinali | 392. |
61Ndi ena pakati pa ansembe anali awa:
62Amenewa anafufuza mayina awo mʼbuku lofotokoza mbiri ya mafuko awo, koma mayinawo sanawapezemo, choncho anawachotsa pa unsembe ngati anthu odetsedwa pa zachipembedzo. 63Bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo mpaka atapezeka wansembe wodziwa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu.| Zidzukulu za |
| Hobiya, Hakozi, ndi Barizilai (Zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai. Barizilai ameneyu ndi uja anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi ndipo ankadziwika ndi dzina la bambo wawoyo.) |
64Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 42,360, 65kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito awo aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Analinso ndi amuna ndi akazi oyimba nyimbo okwanira 200. 66Anali ndi akavalo 736, nyulu 245, 67ngamira 435 ndi abulu 6,720.
68Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale. 69Anapereka kwa msungichuma wa ntchitoyo molingana ndi mmene aliyense chuma chake chinalili: golide wa makilogalamu 500, siliva makilogalamu 2,800 ndi zovala za ansembe zokwanira 100. 70Ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmidzi ya makolo awo.
Copyright information for
NyaCCL