‏ Joshua 12

Mayina a Mafumu Ogonjetsedwa

1Aisraeli anagonjetsa dziko lonse la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni mpaka ku phiri la Herimoni pamodzi ndi dera lonse la kummawa kwa Araba. Iwo anatenga dzikoli kukhala lawo, ndipo mafumu a dzikoli anali awa:

2Sihoni mfumu ya Aamori,

amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi.
3Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga.

4Ogi mfumu ya mzinda wa Basani,

amene anali mmodzi mwa otsala mwa Arefaimu. Iye ankakhala ku Asiteroti ndi Ederi.
5Dera la ufumu wake linafika ku phiri la Herimoni, ku Saleka ndi dziko lonse la Basani mpaka ku malire ndi anthu a ku Gesuri Makati. Ufumu wake unaphatikizanso theka la Giliyadi mpaka ku malire a mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.

6Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisraeli anawagonjetsa ndipo anapereka dziko lawo kwa anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti chikhale cholowa chawo.

7Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo. 8Dziko limeneli linali dera la ku mapiri, chigwa cha kumadzulo, chigwa cha Yorodani, ku matsitso a kummawa, ndi dziko la chipululu la kummwera. Amene ankakhala mʼdzikoli anali Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu ake anali awa:

9
Kuti mukonze bwino tebulo lomwe lili m’vesili, pakhala kofunika kusuntha za vesi (ma) 10-Jos 12:24 m’menemo.
mfumu ya Yeriko imodzi
mfumu ya Ai (kufupi ndi Beteli imodzi
(10) mfumu ya Yerusalemu imodzi
mfumu ya Hebroni imodzi
(11) mfumu ya Yarimuti imodzi
mfumu ya Lakisi imodzi
(12) mfumu ya Egiloni imodzi
mfumu ya Gezeri imodzi
(13) mfumu ya Debri imodzi
mfumu ya Gederi imodzi
(14) mfumu ya Horima imodzi
mfumu ya Aradi imodzi
(15) mfumu ya Libina imodzi
mfumu ya Adulamu imodzi
(16) mfumu ya Makeda imodzi
mfumu ya Beteli imodzi
(17) mfumu ya Tapuwa imodzi
mfumu ya Heferi imodzi
(18) mfumu ya Afeki imodzi
mfumu ya Lasaroni imodzi
(19) mfumu ya Madoni imodzi
mfumu ya Hazori imodzi
(20) mfumu ya Simuroni Meroni imodzi
mfumu ya Akisafu imodzi
(21) mfumu ya Taanaki imodzi
mfumu ya Megido imodzi
(22) mfumu ya Kadesi imodzi
mfumu ya Yokineamu ku Karimeli imodzi
(23) mfumu ya Dori ku Nafoti Dori imodzi
mfumu ya Goyini ku Giligala imodzi
(24) mfumu ya Tiriza imodzi
  mafumu onse pamodzi analipo 31.

10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24
Copyright information for NyaCCL