Nehemiah 7
1Khoma linamangidwa ndipo zitseko zinayikidwa. Pambuyo pake alonda a Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo ndiponso Alevi anasankhidwa. 2Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena. 3Ine ndinawawuza kuti, “Musalole kuti zipata za Yerusalemu zitsekulidwe mpaka dzuwa litatentha, ndipo alonda asanaweruke aonetsetse kuti atseka zitseko ndi kuzipiringidza. Musankhe alonda pakati pa anthu okhala mu Yerusalemu, ena akhale pa malo pawo ndi ena akhale moyangʼanana ndi nyumba zawo.”Mndandanda wa Anthu Oyamba Kubwera Kuchokera ku Ukapolo
4Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe. 5Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo: 6Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerera kuchokera ku ukapolo amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawatenga ukapolo. Iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake. 7Anabwera pamodzi ndi atsogoleri awa: Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana.Tsono chiwerengero cha anthu a ku Israeli chinali chotere:
8 ▼
9– 10– 11– 12– 13– 14– 15– 16– 17– 18– 19– 20– 21– 22– 23– 24– 25– ▼Kuti mukonze bwino tebulo lomwe lili m’vesili, pakhala kofunika kusuntha za vesi (ma) 9-Neh 7:25 m’menemo.
| Zidzukulu za Parosi | 2,172 |
| (9) Zidzukulu za Sefatiya | 372 |
| (10) Zidzukulu za Ara | 652 |
| (11) Zidzukulu za Pahati-Mowabu (kudzera mu mʼbado wa Yesuwa ndi Yowabu) | 2,818 |
| (12) Zidzukulu za Elamu | 1,254 |
| (13) Zidzukulu za Zatu | 845 |
| (14) Zidzukulu za Zakai | 760 |
| (15) Zidzukulu za Binuyi | 648 |
| (16) Zidzukulu za Bebai | 628 |
| (17) Zidzukulu za Azigadi | 2,322 |
| (18) Zidzukulu za Adonikamu | 667 |
| (19) Zidzukulu za Abigivai | 2,067 |
| (20) Zidzukulu za Adini | 655 |
| (21) Zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) | 98 |
| (22) Zidzukulu za Hasumu | 328 |
| (23) Zidzukulu za Bezayi | 324 |
| (24) Zidzukulu za Harifu | 112 |
| (25) Zidzukulu za Gibiyoni | 95. |
26 ▼
27– 28– 29– 30– 31– 32– 33– 34– 35– 36– 37– 38– ▼Kuti mukonze bwino tebulo lomwe lili m’vesili, pakhala kofunika kusuntha za vesi (ma) 27-Neh 7:38 m’menemo.
| Anthu a ku Betelehemu ndi Netofa | 188 |
| (27) Anthu a ku Anatoti | 128 |
| (28) Anthu a ku Beti-Azimaveti | 42 |
| (29) Anthu a ku Kiriati Yeyarimu Kefira ndi Beeroti | 743 |
| (30) Anthu a ku Rama ndi Geba | 621 |
| (31) Anthu a ku Mikimasi | 122 |
| (32) Anthu a ku Beteli ndi Ai | 123 |
| (33) Anthu a ku Nebo winayo | 52 |
| (34) Ana a Elamu wina | 1,254 |
| (35) Zidzukulu za Harimu | 320 |
| (36) Zidzukulu za Yeriko | 345 |
| (37) Zidzukulu za Lodi, Hadidi ndi Ono | 721 |
| (38) Zidzukulu za Senaya | 3,930. |
39 ▼
40– 41– 42– ▼Kuti mukonze bwino tebulo lomwe lili m’vesili, pakhala kofunika kusuntha za vesi (ma) 40-Neh 7:42 m’menemo.
Ansembe anali awa: | A banja la Yedaya (ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa) | 973 |
| (40) Zidzukulu za Imeri | 1,052 |
| (41) Zidzukulu za Pasi-Huri | 1,247 |
| (42) Zidzukulu za Harimu | 1,017. |
45Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:
| Zidzukulu za | |
| Salumu, Ateri, Talimoni, Hatita ndi Sobai | 138. |
46 ▼
47– 48– 49– 50– 51– 52– 53– 54– 55– 56– ▼Kuti mukonze bwino tebulo lomwe lili m’vesili, pakhala kofunika kusuntha za vesi (ma) 47-Neh 7:56 m’menemo.
Anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu anali awa: | Zidzukulu za |
| Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti, |
| (47) Zidzukulu Kerosi, zidzukulu za Siya, zidzukulu za Padoni |
| (48) Zidzukulu za Lebana za Hagaba, ndi za Salimayi, |
| (49) Zidzukulu za Hanani, zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, |
| (50) Zidzukulu za Reyaya, zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nehoda, |
| (51) Zidzukulu za Gazamu, zidzukulu za Uza, zidzukulu za Paseya, |
| (52) Zidzukulu za Besai, zidzukulu za Meunimu, zidzukulu za Nefusimu, |
| (53) Zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri, |
| (54) Zidzukulu za Baziliti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa, |
| (55) Zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema |
| (56) Zidzukulu za Neziya, ndi zidzukulu za Hatifa. |
57 ▼
58– 59– 60– 61Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi.▼Kuti mukonze bwino tebulo lomwe lili m’vesili, pakhala kofunika kusuntha za vesi (ma) 58-Neh 7:60 m’menemo.
Zidzukulu za antchito a Solomoni: | Zidzukulu za | |
| Sotai, zidzukulu za Sofereti, zidzukulu za Perida | |
| (58) zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli, | |
| (59) zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu | |
| zidzukulu za Pokereti-Hazebaimu ndi zidzukulu Amoni. | |
| (60) Anthu onse ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za antchito a Solomoni analipo | 392. |
63Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa: zidzukulu za
Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai (munthu amene anakwatira mwana wamkazi wa Barizilai wa ku Giliyadi ndipo amatchedwa dzina limenelo).
64Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo. 65Choncho bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya china chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mpaka patapezeka wansembe wodziwa kugwiritsa bwino ntchito ya Urimu ndi Tumimu.
66Chiwerengero chonse cha anthuwa chinali 42,360. 67Kuwonjezera pamenepa panali antchito awo aamuna ndi aakazi 7,337 ndiponso anthu aamuna ndi aakazi oyimba nyimbo okwanira 245. 68Panali akavalo 736, abulu angʼonoangʼono 245. 69Ngamira zawo zinalipo 435 ndipo abulu analipo 6,720.
70Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530. 71Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250. 72Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67.
73Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo.
Ezara Awerenga Malamulo
Pofika mwezi wachisanu ndi chiwiri Aisraeli onse anali atakhazikika mʼmizinda yawo.
Copyright information for
NyaCCL