Acts 12
Petro Apulumuka Mʼndende
1Inali nthawi yomweyi imene mfumu Herode anamanga ena a mu mpingo ndi cholinga chakuti awazunze. 2Iye analamula kuti Yakobo mʼbale wa Yohane, aphedwe ndi lupanga. 3Ataona kuti zimenezi zinakondweretsa Ayuda, anawonjeza ndi kugwiranso Petro. Izi zinachitika pa nthawi ya Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti. 4Atamugwira Petro, namutsekera mʼndende, anamupereka kwa magulu anayi a asilikali kuti amuyangʼanire, gulu lililonse linali ndi asilikali anayi. Herode anafuna kumuzenga mlandu pamaso pa anthu onse chikondwerero cha Paska chitapita.5Kotero Petro anasungidwa mʼndende, koma mpingo unamupempherera kolimba kwa Mulungu.
6Usiku woti mmawa mwake Herode amuzenga mlandu, Petro amagona pakati pa asilikali awiri, atamangidwa maunyolo awiri, ndiponso alonda atayima pa khomo. 7Mwadzidzidzi mngelo wa Ambuye anaonekera ndipo kuwala kunawunika mʼchipindamo. Mngeloyo anamugwedeza Petro mʼnthiti ndi kumudzutsa. Iye anati, “Fulumira, imirira!” Ndipo maunyolo anagwa kuchoka mʼmanja a Petro.
8Kenaka mngelo anati kwa iye, “Vala zovala ndi nsapato.” Ndipo Petro atachita izi mngeloyo anamuwuzanso kuti, “Funda chovala chako ndipo unditsate.” 9Petro anatsatira natuluka mʼndende, koma sanazindikire kuti zimene mngeloyo amachita zimachitikadi; iye amaganiza kuti amaona masomphenya. 10Iwo anadutsa gulu loyamba ndi lachiwiri la asilikali ndipo anafika pa chitseko chachitsulo cholowera mu mzinda. Chitsekocho chinatsekuka chokha ndipo anadutsa. Pamene anayenda kutalika kwa msewu umodzi, mwadzidzidzi mngelo uja anachoka.
11Pamenepo Petro anazindikira nati, “Tsopano ndikudziwa mosakayika kuti Ambuye anatuma mngelo wake kudzandipulumutsa mʼmanja mwa Herode, ndi ku zoyipa zonse zimene Ayuda amafuna kundichitira.”
12Atazindikira zimenezi anapita ku nyumba ya Mariya amayi ake a Yohane, wotchedwanso Marko, kumene kunasonkhana anthu ambiri ndipo amapemphera. 13Petro anagogoda pa chitseko cha panja, ndipo mtsikana wantchito dzina lake Roda anabwera kuti adzatsekule chitseko. 14Atazindikira mawu a Petro anakondwa kwambiri ndipo anabwerera osatsekula ndipo anafuwula kuti, “Petro ali pa khomopa!”
15Anthuwo anati kwa iye, “Wopenga iwe!” Atalimbikira kunena kuti zinali zoona, iwo anati, “Ameneyo ndi mngelo wake.”
16Koma Petro anapitiriza kugogoda ndipo atatsekula chitseko ndi kumuona, anthuwo anadabwa kwambiri. 17Petro anakweza dzanja ndi kuwawuza kuti akhale chete ndipo anawafotokozera mmene Ambuye anamutulutsira mʼndende. Iye anati, “Uzani Yakobo ndi abale ena za zimenezi.” Kenaka anachoka napita kumalo ena.
18Pamene kunacha kunali phokoso lalikulu pakati pa asilikali, iwo anafunsa kuti, “Kodi chamuchitikira Petro ndi chiyani?” 19Herode atamufunafuna ndipo wosamupeza, anawafunsa asilikali ndipo analamulira kuti asilikaliwo aphedwe.
Imfa ya Herode
Kenaka Herode anachoka ku Yudeya ndi kupita ku Kaisareya ndipo anakhala kumeneko kwa kanthawi 20Herode anakwiyira anthu a ku Turo ndi Sidoni; anthuwo anagwirizana zoti akambirane naye. Atapeza thandizo kuchokera kwa Blasito, wantchito wokhulupirika wa mfumu, anapempha kuti pakhale mtendere, chifukwa dziko lawo limadalira dziko la mfumuyo pa chakudya chawo.21Pa tsiku limene anasankha Herode, atavala zovala zake zaufumu, anakhala pa mpando wake ndipo anayankhula kwa anthuwo. 22Anthuwo anafuwula nati, “Amenewa ndi mawu a mulungu osati a munthu ayi.” 23Nthawi yomweyo mngelo wa Mulungu anamukantha chifukwa sanapereke ulemu kwa Mulungu ndipo anadyedwa ndi mphutsi nafa.
24Koma Mawu a Mulungu anapitirirabe kufalikirafalikira.
25Barnaba ndi Saulo atamaliza ntchito yawo anachoka ku Yerusalemu, atatenga Yohane wotchedwanso Marko.
Copyright information for
NyaCCL